Chogong'ola dancehall master
Umodzi music
👋👋👋👋👋
08/06/2021
All we asked for was an album and he has already dropped 4 fire hits that are dominating the streets.
NKATIMO is both a club banger and a street anthem that a day can't go by without "Mukununkhira Ndi Nkatimo" phrase mmakwalala mu🙌.
Zaine, a song he did for LCB studios is also trending in different parts of the country making it his second 2021 hit song.
Bwanji by Gwamba featuring Martse nyimbo yomwe anthu amaikakira k*ti siikhalitsa ndi ija pano ikuyaka moto mpaka malo omwera misozi ya ng'ona ija 😂.
The least trending is , nyimbo ya bho chabe vibe ya Nkatimo ija ili untouchable 🗣️.
This is Martse, once the most controversial artist until Waxy Kay and Rash-Ley came in 😁. The Lilongwe based artist promised us an album ndipo ife kumastand kuno Mtima suli mmalo..
KOMA AKADZANGOPALA MTENDERE SADZAUPEZA 😂😂
🔥
30/04/2021
IYI NDI NKHANI YOKHUDZA KOMANSO YONVETSA CHISONIBKWAMBIRI YA MNYAMATA YEMWE MUKUMUONAYI.
Mlembi wa nkhaniyi ndi "Aubrey That'sDhe Boss".
Nkhaniyi ikakhuza moyo wanu chonde muipangeko kuma group omwe mulinao.
Mnyamata adali munthu wanzeru kwambiri panthawi yomwe adali pa sukulu, ndipo ankachita bwino kuyambira ku primary mpaka anaisira mu form 3 panthawi yomwe bambo ake adamwalira.
Zidali zonvetsa chisoni kwambiri kwa imfa yabambo ake omwe sanadwale. Bamboyi adasiya ana awiri tsikana ndi nyamata komanso mayi.
Chifukwa choti mayi ake adali adali osauka adaganiza zosiya sukulu k*ti apitirize mlongo wake ndipo zidayamba kuchitika. Tsikanao anaphunzira mpaka kufika form 4, ak*ti pasala myezi iwiri k*ti alembe mayeso ake a form 4, anayamba kudwala ndipo patadutsa ma week awiri tsikanao anamwaliraso, mayi komanso mlongo wake watsikanai adali okhumudwa kwambiri k*ti chimawachitikira anthuwa chidali chani.
Mayi adasautsika ndi mtendere wamu mtima ndipo ataika maliro amwana waoyo nkudutsa masiku awiri mayi ujaso adazipha namwaliraso pomwepo.
Apa zidali zonvetsa chisoni ndipo mudzi wonse unakhumudwa ndizomwe zinkachitika pabanjali.
Nyamata chifukwa chosautsika ndi mtendere wamu mtima adapenga misala ndipo ndalama zonse zimayenera kupita kwanyamatayi zamaliro amayi ake komanso mlongo wake k*ti athandizikire nazo koma chifukwa choti anapenga misala anthu anamutengera ku mental komwe ndalamazo amamulipirira.
Ku mental-ko adakhalako mpaka zaka 4 asanachire, muchaka chachisanu (5) ndipomwe anachira.
Atabwerakako kuchipatala kuja panalibe munthu yemwe anamulandira ngakhale achibale ake ankangomuyang'ana ndipo ena kumusala.
Sadalimbane ndi munthu aliyense kumuvutitsa k*ti azimusunga koma adayamba kupephetsa ndipo anthu ena ankamuthandiza zomwe amakwanitsa kulipira nyumba ya Mwk1,500 pamwezi ulionse kwa myezi iwiri.
Alinkati mopephetsa muja zinthu zidasiya kuyamba kumuyendera ndipo amathano mwezi uja Mwk1,500 osaipeza zomwe zidapangitsa ainu nyumba kumuthamangitsamo.
Inu zidali zonvetsa chisoni ndi moyo wanyamatayi. 😭😭😭😭😭😭😭
Nyamatayi adafika pozifusa kwa Mulungu k*ti "kodi iyeyu adalakwitsa chani zomwe zikumpqngitsa kusowa mtendere padziko lapansiri, kodi Mulungu anthu osaukafe tidalakwanji ife? Kapena dzikoli mudapereka kwa anthu achuma? "
Awa adali mafunso omwe nyamatayi amazifusa ndipo adafika pofuna kungozipha kodi adazindikira mwachangu k*ti kuzipha mphoto lake ndikumoto ndipo sadapangeso zozipha.
Atamutulutsa munyumba muja adayambano kugona pansi pa bridge ndadzuka kukacha ulendo wokapephetsa.
Mwamwayi tsiku lina anatola phone ndipo chifukwa choti kasukulu kadalimo m'mutumo adaganiza zolowako pa Facebook ngati njira imodzi yofuna kupepherako chithandizo.
Analowa pa Facebook nayamba kupepha chithandizo cha Mwk30,000 k*ti akufuna kwabwino amuthandize koma ayi ndithu, olo m'modzi comment, anayesesa k*tumiza m'magroup osiyanasiyana koma palibe ndim'modzi yemwe adamuyakhako ndipo mwangozi tsiku lina akugona pansi pa bridge nvula inayamba ndipo phone ija inanyowa ndikuonongekera pompo.
Nyamatayi sadafoke koma adalemba makalata okwana 30 opepha chithandizo omwe adawatumiza kwazibale ake ndipo mwa anthu 30 atatu okha ndiomwe adamuyakha, ndipo mwaatatumo adamulonjeza k*ti amuthandiza adali awiri, koma mwa awirimo palibepo yemwe adakwaniritsa lonjezeyo.
Moyo nyamata unamupweteka ndipo ankangokhalira kulira tsiku ndi tsiku.
Apano zithu zinamufika ndipo akapephetsano anthu ankamuyakha motere: anzako aliku orphan aise osangopita konko bwanji!
Ena ankati, tiribe ndalama ife ukakhala umphawi ndiwako anzako akugwira maganyu kunjaku,
Enaso ankati, pita ukabe akak*tsekere uzikadya ya boma ku prison.
Inu izi zidali zokhudza ndithu olo muli inu mudakatani????
Tsiku lina akugona pansi pa bridge Truck ikudutsa idachita ngozi ndipo bridge yo idagumuka ndikunkugwera nyamatao ndipo adamwaliriraso pomwepo.
😭😭😭😭😭😭😭😭😭😭😭😭😭
Rest In Peace..
Kunja k*tacha anthu adapeza mtembowo ndipo anthu adamuzindikira mosavuta kamba kakupephetsa.
Mwambo okaika maliro utakwana, anthu akumpingo omwe mayi ake amapepherako adapereka ndalama zokwana Mwk300,000,
Akuchimuna atasokhasokha adaperekaso Mwk450,000, mzimayi yemwe adamuthamangitsa rent uja adapereka Mwk100,000 ndipo atatolera yochopereka idakwana Mwk50,000.
Ndipo azibale ake akuchikazi adaperekaso ndalama yokwana Mwk200,000.
Ndalama zonse idakwana 1.1 Million.
Anthu adagula bokosi yodula ija ya Mwk450,000.
Kudali mphwando ndipo kudafa ng'ombe ndi mbuzi mpuka ngati zomwe zidatenga ndalama yokwana Mwk 500, 000.
Ili ndiye dziko lapansi lomwe limaonetsa chikondi komanso kukoma mtipa kwa munthu yemwe watisiya akakhala ku gulu la anthu. Kodi ndalama zonsezi zidakakhala k*ti anampatsa panthawi yomwe adali moyo kodi adakamwalira?
Ilitu nditsoka komanso ntchimo lalikulu pamaso pa Mulungu ndipo Yehova akuona.
Inuso k*thekera kothandiza munthu wina wake mulinako koma taonaonani zomwe mumapanga? Nthawi yothandiza amasiye komanso ozunzika mulibe, ndipo mumati zomwe mumapeze ndizochepa, kodi simukudziwa k*ti mutamudalitsa wina wake ndikochepa komwe mulinako ndipo k*thokoza kwake kukhoza kukhala m'dalitso pamoyo wanu?
Ndi Mwk1,000 yomweo mdzadalitseni nayo wina wake mudzaone zomwe Mulungu adzapange ndi moyo wako, ndi sukulu yako, ndintchito yako, ndi mwamuna/mkazi wako, ndi banja lako, ndinthenda yako komanso moyo wako wauzimu!
Kodi sumudabwa k*ti ndichifukwa chani chipepherere moyo wako ndizosowa zako sizikuyakhidwa?
Mulungu angakudalitse bwanji usakudalitsa ena? Sukuona anthu kunjaku akuzunzika?
Deya amene ena sakukwanitsa kumupeza kunjaku.
Mulungu akukhudzeni lero nakupatsani mtima wachisoni.
Ndikudziwa k*ti uthengau wakukhudzani ndipo mwazisomo za Ambuye mupangako share Nkhaniyi kuma group atatu okha.
Muthaso ku join nafe group yamau auzimu pa WhatsApp
+265994917253 Komatu group ya anthu ofuna moyo wao wauzimu kukwera.
On Facebook group
https://facebook.com/groups/150396872450702
Mlembi wa nkhaniyi ndi "Aubrey That'sDhe Boss"
17/03/2021
Uyu ndi THIN DICON
amene Ali mu achaida universe
Ambiri mukumudziwa ngati munavelako nyimbo ya ULERE
amadisa LORD GAGA
Emwe amakhala Ku l city Ku 23 Ku tank
17/03/2021
Uyu ndi thin dicon ambiri mukumudziwa Ali my achairda universe
Thanks people like this Page 🎵🎧💦💎
MUMOWA MULI NYAMA YOGAYAGAYA
INE MU DANCEHALL NDINE LION
12/02/2021
Norman Chisale mulandu nambala 4 out of 24. ..
Lero Norman Chisale wapezekaso ndimulandu olowesa magalimoto amtundu wa Landilova okwana asanu ndiawili posakhomera msokho wina uliose. .
Chisale wakwanisa mulandu yokwana 4 kufikila pa mwamba pamilandu ina monga ofuna kapha nzimayi pomuombera pamwendo, mulandu wa saga simenti komaso okupha mwakhaza nkulu wakale wa ACB isa jaunju ndikumuika musaka nkukamukwilila munchenga .
Mwapasipasi tinapeza k*t chisale alindimilandu yokwana 24 yomwe anapalamula pomwe anali wankulu wachitetezo cha president wakale wa pita muntharika muulamulilo wa DPP.
Pali malipoti ak*t apolisi aku Lilongwe area 30 akufusa bamboo chisale zamomwe analowesera magalimoto kuchokera ku South Africa ndipo ngati papezeke umboni wazachinyengo apolisi wa akuyembekezeka kulanda magalimotowa ndikuwamanga bambo Chisale.
Kuchokera ku Lilongwe area 30 ndine. C H D 📝👷😷👇
Aneso ndimafuna ntakhala fresh
Samesame like somba ya fresh
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Contact the business
Telephone
Website
Address
1233
Lilongwe
897588
